NationalNews

ABA CHIMANGA CHOGAWIRA ANTHU OSOWA

Mtolankhani wanthu

Pomwe njala yafika povuta ndipo maanja ochuluka akugona kumimba pululu, a Elias Musah, a zaka 40 zakubadwa komanso a Wilson Musah, a zaka 32 ali m’chitokosi cha polisi kaamba kosowetsa matumba a 196 a chimanga.

Mneneri wa Polisi ya Mangochi, Amina Tepani Daudi wati chimangachi chili mu ndondomeko yogawa kwa maanja omwe avutika ndi njala omwe akugawa ndi a nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya Dodma.

A Daudi ati malingana ndi ogwira ntchito ku Dodma ku Mangochi, nthambi-yi inasunga matumba 676 ku Choponde oti agawire anthu.

A Daudu ati pa 28 November 28, komiti idagawa chimanga madera awiri okha, ndipo anthu a dera Lachitatu anauzidwa kuti agawilidwa chimangachi tsiku lotsatila.

Izi akuti zinachititsa ogwira ntchito ku Dodma kusiya matumba 196 kwa awiri oganizilidwawa.

“Atabwelera pa 6 December kuti akagawe chimanga chotsalachi, anapeza kuti mchipinda chomwe anasunga chakudyachi mulibe ndipo oganizilidwa-wa ananama kuti anagawa chimangachi kwa anthu ena omwe sanali pa ndandanda mwa anthu opindula,” atero a Daudi.

Pakali pano awiriwa ali mmanja mwa a polisi ndipo awatsegulira mulandu wakuba ndipo a polisi akuchita kafukufuku kuti apeze matumba obedwa-wa.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *