News

ABAMBO ATATU ACHITA CHOLANDIZANA KUGWILA MZIMAYI KWA MAOLA ANAYI

Cyrus Bengo

Abambo atatu lero agamulidwa kukasewedza ndende yakalavula Gaga kwa dzaka makhumi awiri aliyense bwalo litawapedza ndi mlandu ogwilira mzimayi wa dzaka makhumi atatu, zisanu ndi chimodzi komanso kumulanda ndalama yokwana K I57 000 ku Lililongwe.

Iwo ndi a Yona Maulidi a zaka makhumi atatu zisanu ndi zinayi 39, Owen Legani azaka khumi, zisanu ndi zinayi 19, komanso a William Phillipo a zaka makhumi atatu zisanu ndi zinayi 39. Zikumveka kuti ochitilidwa chiwembu anakumana ndi tsoka ili usiku wapa Febuluwale 18 2022 pomwe ankachokera kunyumba ya wachikondi wake.

Oyimira boma pa milandu Bauleni Namasani anawuza oweludza milandu Rodrick Michongwe anthu atatuwa anali ndi zikwanje komanso zomatsulira misomali ( crowbars) pomwe ankamugwililira mochita cholandidzana kumubanda kucha kwa Kaondo mutawunichipi ya Area 36 .

Namasani anapempha bwalo kuti lipereke chilango chikhwima kuti ena a malingaliro ngati awa atengerepo phunziro , ponena kuti zomwe anapangadzi zopanda umunthu komanso zopepusa mzimayi.

Popereka chigamulo, a Michongwe anati mchitidwe wa anatuwa ndi onyasa. Iwo anapitiriza kupereka chilango chokasewedza ndende kwa makhumi awiri.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *