News

AGAMULIDWA KUGWILA NDENDE KWA ZAKA 20 ATAGWILIRA MZUKULU WAWO

Cyrus Bengo

Zina ukamva kamba anga mwala ku Lilongwe lero bwalo lamilandu lagamula a Kondwani Chitukula a zaka 39 kukakhala kundende ndikukagwila ntchito yakalavula gaga pogwilira mkulu wawo wazaka zinanu ndi zinayi.

Oyimilira boma pa mlanduwu a Vincent Ntalawe anawuza bwalori kuti bambowa anapalamula mlanduwu pakati pa miyezi ya January ndi February 2023.

Iwo anapitiriza kunena kuti mwanayu amakhala limodzi ndi agogo ake a amunawa komanso a akazi . Anthu apadera atawona kuvutika poyenda kwa mwanayu anadya nkhonde komwe anakawulula kuti agogo ake ndi omwe apanga za upanduwu , apa anthu anakawuza makolo a mwanayu omwe anakatula nkhani ku polisi.

Atakayeza kuchipatala , anapeza kuti mwanayu wakhala akugwililidwa kangapo konse, koma agogowa pa bwalo anawukana kwa mutu wa galu kuti sakuziwapo kanthu pa za mlanduwu.

Popereka chigamulo chake Rodrick Michongwe anati mchitidwewu ukula ndipo nkoyenera kupereka chilango chokhwima kuti ena atengelepo phunziro.

Iwo amachokera mdera la mfumu yayikulu Masaula ku Lilongwe.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

One thought on “AGAMULIDWA KUGWILA NDENDE KWA ZAKA 20 ATAGWILIRA MZUKULU WAWO

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *