News

AMAGWIDWA ATAFUKULA MITEMBO YA ANA

Mtolankhani Wanthu

Apolisi ku Phalombe amanga Charles Katunga komanso Amos Magombo ati kamba kopezeka ndi ziwalo za munthu komanso kupezeka ku manda.

Mneneri wa polisi m’bomali Jimmy Kapanga wati pa 2 June chaka chino anatsinidwa khutu ndi munthu wina ochita malonda pa malo pa Migowi kuti anthu awiriwa amagulitsa mitembo iwiri ya makanda.

Izi zidachititsa kuti apolisiwa afike pa malowa ndi kumanga anthuwa.

“Apolisi atapanga chipikisheni anapeza matupi amakandawa omwe achipatala anatsimikiza kuti ndi mapasa koma atayamba kuonongeka ndipo atafunsidwa zinadziwika kuti anakafukula anawa ku manda ena m’mudzi wa Jaden mfumu yayikulu Kaduya m’bomali,” watero Kapanga.

Katunga amachokera m’mudzi mwa Mgona pomwe Magombo amachokera m’mudzi mwa Njaya mfumu yayikulu Kaduya ku Phalombe ndipo awiriwa akaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *