News

AMWALILA ATAMWA MANKHWALA AKUCHIPATALA MOONJEZA

Mtolankhani wanthu

Mayi wa zaka 39 Lizie Kanyotha wamwalira atamwa mankhwala akuchipatala moonjeza muyezo.

Mneneri wa polisi m’bomali Sergeant Tupeliwe Kawilo wati Kanyotha anamwa mankhwalawa pa 12 June chaka chino kudera lomwe amakhala ku Mantchewe mdera la Livingstonia.

Izi akuti zidachitika kutsatila nkangano omwe unalipo pakati pa mayiyu ndi mamuna wake.

“Mamuna wa mkaziyu anadzatula nkhaniyi ku polisi komanso kwa makolo a mkaziyu omwe anamulangiza. Koma izi sizinamusangalatse ndipo atabwerera kunyumba anamwa mankhwalawa ndipo wamwalira Lachitatu pachipatala cha David Gordon Memorial,” watero Kaliwo.

Mayiyu amachokera m’mudzi mwa Kanyotha mfumu yayikulu kachulu ku Rumphi.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *