News

ANTHU AWIRI AWAMANGA KAAMBA KOPEZEKA NDI CHAMBA

Mtolankhani wanthu

Apolisi ku Lilongwe amanga anthu awiri kaamba kopezeka ndi matumba atatu komanso makatoni asanu a chamba omwe amafuna kutumiza ku Blantyre.

M’neneri wa polisi ya Lilongwe Hastings Chigalu wati anthuwa mayina awo ndi Ackim Lameck wa zaka 23 komanso Catherine John wa zaka 30.

Iye wati m’modzi mwa anthu ku kampani yonyamula katundu yomwe anthuwa amafuna kugwiritsa ntchito kutumiza chambachi anawatsina khutu za nkhaniyi.

“Apa, mpomwe apolisiwa anayamba kufufuza nkhaniyi ndipo anamanga Lameck yemwe anali mmalo okwerera bus a Shire. Atapanikizidwa ndi mafunso, Lameck analondolera apolisiwa kwa Mtsiliza komwe anakagwira Catherine atamupeza ndi matumba ena atatu a chamba,” watero Chigalu.

Awiriwa akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa kuti akayankhe mlandu opezeka ndi chamba popanda chilolezo.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

3 thoughts on “ANTHU AWIRI AWAMANGA KAAMBA KOPEZEKA NDI CHAMBA

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *