News

APOLISI AMANGA BAMBO POVULAZA MKAZI KAMBA KA NSANJE

Mtolankhani wanthu

Apolisi ku Nkhotakota amanga bambo wa zaka 32, Ernest Nambazo kaamba kovulaza mkazi wake mmudzi mwa Samuel pomuganizira kuti akuchita chibwenzi cha nseli.

Mneneri wa polisi m’bomali Sergeant Paul Malimwe wati pa 3 July Nambazo anapita ku mowa ndipo pobwera usiku anakumanizana ndi mkazi wake akuchokera ku chimbudzi.

Apa, iye wati Nambazo anafunsa mkaziyo komwe amachokera ndipo ngakhale mkaziyu anafotokoza, sizidanveke ndipo m’malo mwake anati mkaziyu amachokera ku chibwenzi.

“Nambazo analowetsa zala zake ku malo obisika a mkazi wake ati pofuna kutsimikiza ngati wagonana ndi mamuna wina ndipo kutha apo anatenga thabwa nkuyamba kumenya mkaziyu mpaka kumukomola,” watero Malimwe.

Iye watinso anthu akufuna kwabwino ndi omwe anatengera mayiyu ku chipatala komwe anakalandira thandizo.

Nambazo amachokera m’mudzi mwa Samuel Mfumu yayikulu Mwadzama ku Nkhotakota.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

One thought on “APOLISI AMANGA BAMBO POVULAZA MKAZI KAMBA KA NSANJE

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *