NationalNews

ATALI MISINKHU KUMAYENDA MOSAMALA- ATERO AZANYENGO

Cyrus Bengo

Katswiri pa nkhani za nyengo ku nthambi yoona za nyengo ndi kusintha kwa nyengo m’dziko muno, Akimu Phiri wati anthu omwe ndi atali-atali misinkhu akuyenera kumayenda mosamala m’nyengo ya mvula kamba koti amakhala pa chiopsyezo choombedwa ndi mphezi.

Phiri wayankhula izi m’boma la Mchinji pa maphunziro a masiku atatu okhudza za nyengo omwe akonzedwa ndi bungwe la Total Land Care.

Iwo ati pomwe anthu atali-atali akuyenda malo womwe palibe mitengo kapena zinthu zina zitali-zitali chiopsyezo chawo chimakhala chachikulu kamba koti ziphaliwali zimakonda kutsira pa chithu chomwe ndi chotalikirapo.

‘Ukakala kuti ukuyenda pa malo pomwe palibe chithu china chachitali pamene iwe uli wamtali, ndi kofunika kwambiri kuti chiphaliwali chikawomba uzigona pansi’, achenjeza motero a Phiri.

Malinga ndi katswiriyu, chiphaliwali chimakhala ndi nyetsi zochuluka kwambiri zomwe ndi pafupifupi ma digilizi 30,000 chomcho wati anthu akuyenera azisamala malo wokhala nthawi yomwe kukugwa mvula ya ziphaliwali.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *