News

BAMBO ACHITA ZA MATHANYULA NDIKUPATSIRA MATENDA MNYAMATA WA ZAKA 13

Olemba Mtolankhani oyima payekha

Apolisi m’boma la Zomba akusunga mchitokosi bambo wina wa zaka 21, Andrea Nkula pomuganizila kuti amachita zadama ndi mnyamata wa zaka 13.

Malingana ndi mneneli wa polisi m’bomali, Sergent Aaron Chilala, mkuluyi adapalamula mlanduwu pakati pa mwezi wa February ndi March chaka chino.

Izi akuti zidachitika nthawi ya usiku mkazi wake atachokapo kupita ku maliro m’mudzi momwemo. Apa, mkuluyu adapeza mwayi wochita zadama ndi m’nyamatayi m’nyumba mwawo.

“Mkuluyi wakhala akuwopseza mnyamatayi kuti adzamchita zoopsa akadzaulula zochitikazi. Pachifukwachi, mnyamatayu wakhala akumva ululu wochuluka akafuna kuchita chimbudzi, ndipo kenako adafotokozera makolo ake za zomwe zidamuchitikira,” watero Chilala.

Nkhaniyi adakayipeleka m’manja mwa polisi a Kachulu ndipo chipatala chaching’ono cha Likangala chidapeza umboni kuti mnyamatayi adagonedwa ndipo adapezekanso ndi matenda opatsilana pogonana.

Padakali pano, mkuluyi akuyembekezeka kukaonekera kubwalo la milandu. Nkula amachokera m’mudzi mwa Njala, mfumu yaikulu Mkagula m’boma la Zomba.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *