News

BAMBO WAMANGIDWA ATATUMIZA ZITHUNZI ZOLAULA ZA MKAZI WAKE WAKALE

Mtolankhani wanthu

Apolisi m’boma la Chikwawa akusunga mchitokosi bambo wa zaka 25 zakubadwa, a Chris Mbewe powaganizira kuti akhala akutumiza zithunzi zolaula komanso kutukwana mkazi wawo wa kale pa masamba a mchezo.

Malingana ndi wofalitsa nkhani za apolisi m’boma la Chikwawa a Dickson Matemba, odandaulawa omwe ndi a zaka 25 zakubadwa akhala ali paubwenzi ndi mamunayo kwa miyezi khumi ndi umodzi .

“Ndipo ali mkati mwaubwenzi mamunayo anafotokozera mkazi wake kuti akaonekere kwa makolo ake koma mkaziyo atafunsa ndalama yomwe adzagwiritse ntchito pa ulendowu , mamunayi adamuuza kuti abwereke kwa mzake zomwe mkaziyo anakana”, atero a Matemba.

Apa, a Mbewe adakhumudwa ndipo adayamba kumutukwana ku WhatsApp ndipo akuti anatumizanso zithunzi zolaula kwa bambo a mkaziyu zomwe zimaonetsa awiriwa ali mchikondi.

A Matemba ati a Mbewe akaonekera kubwalo la milandu akamaliza kafukufuku wawo. A Mbewe amachokera mudzi wa Julius mudera la Mfumu yaikulu Katunga m’boma la Chikwawa .

Pakadalipano, apolisi m’bomalo achenjeza mchitidwe wotumizira zithunzi zolaula ponena kuti ndikuphwanya malamulo oyendetsera dziko lino komanso ndikuphwanya ufulu wa munthu.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *