News

CDHIB CHITSOGOLO NDI MASEWERO A DARTS

By Andrew Mwanandiye Tembo

Pali chiyembekezo choti masewero a Darts tsopano apita patsogolo potsatira chidwi cha anthu akufuna kwa bwino pa masewerowa mdziko muno.

Izi zadziwika pomwe bank ya CDHIB yapereka cheque cha ndalama zokwana 5 Million Malawi kwacha Ku bungwe la Darts Association of Malawi lachitatu lathali mu mzinda wa Blantyre.

Polakhula pa mwambowu mmodzi mwa akuluakulu oyendetsa ntchito za malonda Ku bankiyi Nancy Bisika anati aganiza zobwera ndi thandizoli potengera kuti masewerowa ndi amodzi mwa masewero omwe akusowekera thandizo lalikulu ngati chilimbikitso cha ndalama Mwa zina chabe.

Nancy Bisika

“Titaona kuti masewero a Darts sakupita patsogolo chifukwa chosowa nthandizo ife a bank tinaganizo zothandizapo

“Ambiri amasakha kuthansiza masewero ena kotero Darts imasewekera zochuluka”.Anatero Bisika.

Apa a Bisika anati ndichokhumba chawo chachikulu ngati bank kuti masewerowa apite patsogolo pofikira anthu ochuluka monga achinyamata ndi amayi kuti nawo azisewera masewerowa mdziko muno.

Polandira thandizoli, mlembi wamkulu Wa bungwe la Darts Association of Malawi Prestone Matande wayamikira bankiyi pobwetsa nthandizoli Ku nthawi yake ponena kuti ndalamazi zithandizira pa mpikisano wa osewera osiyanasiyana omwe uyambike lachisanu pa 22 mwezi uno omwe mafainolo ake adzachitike sabata lomaliza la mwezi woyamba Wa chaka cha mmawa.

Prestone Matande , kumanja

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *