News

JUBEKI NDI SWALI AMAGWIDWA PA MLANDU OKUBA KU MITUNDU

Mtolankhani wanthu

Apolisi ku Mitundu m’boma la Lilongwe amanga abambo awiri kaamba kothyola nyumba ndikuba njinga ya moto ya ndalama zokwana 1.7 miliyoni kwacha.

Mneneri wa Polisi ya Lilongwe, Inspector Hastings Chigalu wati awiriwa ndi a Swali James azaka 40 komanso a Jubeki Lifati azaka 20.

A Chigalu ati akuluakuluwa anathyola nyumba ya a Paul Kalinde pa 03 Okutobala chaka chomwe chino ndikubamo njinga moto yomwe mwini wake anali atangoyigula kumene.

A Lifati komanso a James anakamangidwila ku Kasungu komwe amafuna kukagulitsa njingayi yomwe anakanika kupereka mapepala khumutcha wina atawafunsa kutero.

A Swali James amachokera mudzi mwa Malanga, mfumu yaikulu Masula pomwe a Jubeki Lifati amachokera mmudzi mwa Liwiro mfumu yaikulu Chadza onse a m’boma la Lilongwe.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *