News

MA QUEENS AYITANIDWA KU DZIKO LA AUSTRALIA

Olemba Cy’rus Bengo

Timu ya mpira wamanja ya dziko lino yaitanidwa kukachita nawo mpikisano wotchedwa PacificAuss Netball Series omwe ukuyembekezeka kukachitikira mumzinda wa Queensland ku Australia.

Ma Queens kusangalala atawina m’mbuyomu

Bungwe Ioyang’anira masewerowa mdziko muno Ia NAM Iati uwu ndi mwayi oti timu ya fukoyi ikaone muyeso wa mphamvu zake pomwe ikukonzekera masewero a Netball World Cup omwe adzachitike ku South Africa mu July chaka chino.

Mpikisano wa PacificAuss Netball Series umabweretsa pamodzi maiko omwe ndi zilumba za m’nyanja yamchere ya Pacific ukhala wachitatu kuchitika chikhazikitsireni.

Chaka chino, akuluakulu okonza masewerowa aitana maiko atatu a ku Africa omwe ndi Malawi, Zambia ndi Kenya kuti akapikitsane nawo.

Masewerowa adzachitika kumapeto kwa mwezi wa April kuyambira pa 24 mpaka 29 ndipo maiko okwana asanu ndi atatu ndi omwe akuyembekezeka kutenga nawo mbali.

Malinga ndi maere omwe achitidwa, Queens ili mu gulu loyamba. MaguIu onse ali motere:

Pool A
Malawi πŸ‡²πŸ‡Ό
Samoa Islands πŸ‡²πŸ‡­
Fiji πŸ‡«πŸ‡―
Papua New Guinea πŸ‡΅πŸ‡¬

Pool B
Tonga Islands πŸ‡ΉπŸ‡΄
Kenya πŸ‡°πŸ‡ͺ
Zambia πŸ‡ΏπŸ‡²
Singapore πŸ‡ΈπŸ‡¬

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *