NationalNews

MAI AMUMANGA ATAGWILILIRA MNYAMATA

Mtolankhani wanthu

Mai wa zaka 31, Naomi Ngwira amunjata m’boma la Rumphi pomuganizira kuti adachita za dama ndi mnyamata wa zaka 14.

Mneneri wa apolisi m’bomali, Noel Kamchenga wati izi zidachitika pa malo ochitira malonda a Chitimba pa 20 November chaka chino

Nkhaniyi ikuti maiyu adanyengelera mnyamatayu kuti amupelekeze ku nkhalango kotola nkhuni.

Kamchenga wati ali kumeneko, mayiyu adakakamiza mnyamatayu kugona naye ndipo adamuopseza kuti asawulule kwa aliyense.

“Koma kenaka mnyamatayu adayamba kusamva bwino mthupi. Atapita naye ku chipatala cha Chitimba adamupeza ndi chizonono,” watero Kamchenga.

Atamufunsa, mnyamatayu akuti adaulula kuti adagonana ndi a Ngwira mosadziteteza.

Apa, apolisi adamanga mayiyu yemwe akuyembekezeka kukaonera ku bwalo la milandu komwe akayankhe mulandu ogonana ndi mwana zomwe ndi zosemphana ndi gawo 132 (2) la malamulo a upandu.

Naomi Ngwira amachokera m’mudzi mwa Mwabongolo, mfumu yaikulu Mwalweni m’bomali.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *