News

MAI WINA WAPEZEKA ATAFA KU LILONGWE

Mtolankhani wanthu

Apolisi ku Lilongwe ati apeza thupi la mzimayi kuseli kwa Gateway .all lomwe akuliganizira kuti ndi la mayi wina yemwe dzina lake ndi Agnes Katengeza yemwe adasowa Loweruka pa 23 September.

Mneneri wa polisi ya Lilongwe Hastings Chigalu wati pakadali pano kafukufuku ali nkati pofuna kutsimikiza ngati thupili lilidi la Katengeza.

Chigalu wati anthu adikirebe pang’ono kuti athe kupeza chenicheni pa nkhaniyi kudzera mwa a chipatala.

”Titsimikize kuti tapeza thupi la mzimayi kuseri kwa Gateway Mall ku Lilongwe ndipo pakadali pano tikuchita kafukufuku pa zinthu zingapo kuphatikizapo kuti tidziwe chomwe chapha mayiyu,” watero Chigalu.

Iye watinso thupi la mayiyu lapezeka mu galimoto koma pakadali pano nkovuta kutsimikiza ngati wachita kuphedwa kapena ayi komanso ngati ali mzimayi yemwe wakhala akulengezedwa kuti wasowayo.

Koma mlongo wake wa Agness, Hexin Katengeza watsimikiza kuti thupi la m’bale wake lapezeka ndi mabala ooneka kuti wachita kuphedwa ndikumponya kumbuyo kwa galimoto yake.

Iye wati poti nkhaniyi ili mmanja mwa apolisi sangafotokozepo zambiri.

Malipoti ngati awa akuchulukira ku Lilongwe pomwe sabata yatha m’modzi mwa akuluakulu ku kampani ya Coca-Cola Beverages anapezekanso ataphedwa mgalimoto yake.

Izi zikudzetsa mantha pakati pa anthu okhala mu mzindawu maka pa nkhani ya chitetezo.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

One thought on “MAI WINA WAPEZEKA ATAFA KU LILONGWE

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *