News

CHISWEMBWERE CHANYANYA PA CHIPATALA CHA MWANZA -MFUMU YADANDAULA

Mtolankhani wanthu

Mfumu yaikulu Nthache ya m’boma la Mwanza yati nchitidwe wa chiwerewere pakati pa atsikana oyendayenda, ena mwa anthu oyedetsa galimoto onyamula katundu komanso anthu ochita malonda pakati pa dziko lino ndi maiko ena kudzera ku chipata cha Mwanza wakula kwambiri.

Mfumu Nthache yati kukhalitsa kwa anthu ochita malonda pa chipata cha Mwanza pamene akufuna kuombola katundu wawo ndi zina mwa zifukwa zomwe zikukolezera mchitidwewu.

“Amuna ena amakhala pano akudikilira mapepala akatundu wawo mpaka sabata imodzi ndiye akaona nkazi samapilira koma kuchita naye zadama. Atsikanawa panopa anabwelera nkhani yake yomweyo ndiye amangoti laponda la mphawi,” inatero mfumu Nthache.

Komabe mfumuyi yati ntchito yomanganso chipata cholowa ndi kutuluka mdziko muno cha Mwanza yotchedwa One Stop Border Post pa chigerezi yomwe cholinga chake ndi kufuna kuti anthu ochita malonda komanso onyamula katundu asamazadikire nthawi yaitali kutenga mapepala a katundu wawo ikazatha izathandiza kuchepetsa nchitidwe wachiwerewere-wu

Pakadalipano tapeza kuti ena mwa oyendetsa galimoto za mtundu wa truck nthawi zina amatha kukhala pamalowa kwa sabata imodzi akudikilira kuti galimoto zawo zilandire mapepala olowera mdziko muno.

Boma ndi ndalama zokwana K3.2 billion likumanga malo otchedwa One Stop Border Post ku Mwanza ndipo mwazina cholinga chake ndikutukula ntchito za malonda pochepetsa nthawi yomwe eni katundu amadikira pa malowa

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *