News

MFUMU ISEWERETSA MALO OBISIKA A MSUNGWANA

Mtolankhani wanthu

Anthu m’boma la Dowa akupukusa mitu yopanda miyanga zitadziwika kuti mfumu M’bwatamila ayinjata ati kaamba kogwira ndi kuseweretsa maliseche a msungwana wa zaka khumi nkumupaka ufa wakuda kumalo obisika.

Mneneri wa polisi m’bomali, Alice Sitima wati mfumuyi ndi ya zaka 71 zakubadwa ndipo akuyiganizira kuti idachita malodzawa ku nyumba yake dzulo, Lachisanu.

Mfumuyi yomwe dzina lake leni Leni ndi Chisoni Basiketi, akuti patsikuli adakumana ndi msungwanayu pamodzi ndi a mzake ena pomwe amapita kokatchyola ndiwo za masamba ku dimba.

Mfumu M’bwatamila

“Madzulo ake, mfumuyi idayitana asungwanawa m’modzi-m’modzi kuti alowe munyumba mwake,” watero Sitima.

Sitima wati pomwe msungwana ochitidwa chipongweyu analowa m’nyumbamo, mfumuyi idatseka chitseko. Kenaka, idakakamiza mwanayu kuvula chovala chake cha mkati.

Apa, mkuluyu akuti adayamba kugwira msungwanayu ku maliseche kwinaku akumamupaka zinthu zakuda pa malowo.

Zitadziwika, anthu adatengera msungwanayu ku chipatala cha Dowa. Atamuyeza, adapeza zinthu zokudazi ku maliseche ake komanso akuti amatuluka magazi ku malowa.

Izi zidapangitsa apolisi kumuthira unyolo mkuluyu ndipo amutsekulira mulandu oseweretsa msungwanayu ku malo obisika monyazitsa komanso kumuchotsera ulemu.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *