News

MIYEZI 8 KU NDENDE ATAGAWA ZINTHUZI ZOLAULA

Cyrus Bengo

Bwalo la milandu ku Chikwawa lagamula bambo wa zaka 25 Christopher Mbewe kuti alipire chindapusa cha K400,000 kapena kukakhala ku ndende miyezi 8 kamba kogawa zithunzi zolaula za mkazi yemwe anali naye pa ubwenzi pa masamba a mchezo.

Oyimira boma pa mlandu ku Chikwawa Sub Inspector Emmanuel Namarwa anati zomwe anachita Mbewe ndikupanda umunthu komanso anazunza kaganizidwe ka mkaziyo poganizira kuti zithunzizo zinafikanso kwa bambo a mkaziyu.

Mbewe anavomera mlanduwu koma anapempha bwaloli kuti limuganizire kamba koti nkoyamba kupalamula komanso ali pa sukulu.

Pakadalipano, Mbewe sanapereke ndalamayo ndipo amutumiza ku ndende ya Chikwawa. Mbewe amachokera mmunmdzi mwa Julius mfumu yayikulu Katunga ku Chikwawa.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *