News

Mtumiki, Clifford Kawinga athandiza anthu ndi chakudya.

Apostle Clifford Kawinga yemwe ndi mtumiki wa Salvation for all Ministries international lero afikira ndi chakudya anthu oposera 2000 omwe akhuzidwa ndi njala m’boma la Thyolo.

Apostle Kawinga ayamba mwambowu ndikugawira anthu uthenga wa Mulungu okhudza kutembenuka mtima ndi kubadwa mwatsopano mwa Khilistu Yesu.

Apostle Kawinga ati anachita izi pofuna kukwaniritsa nsanamira ya utumiki wawo pothandiza anthu pa moyo wa kuthupi powapasa chakudya, ndi kuthandiza ku moyo wa uzimu powalalikira uthenga wa chipulumutso ochokelera m’baibulo.

Wina mwa katundu yemwe apereka ndi monga chimanga, bread ndi wina ndipo mwambowu unachitikira pa bwalo lotchedwa Dzimbiri, lomwe likupezeka m’dera la mfumu yaikulu Mphuka, ku dera la Thyolo Thava.

By Freshmade Mw

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *