Uncategorized

MUSEVENI WAKANA MATHANYULA KU UGANDA

Mtolankhani wanthu

Malipoti a nyumba zosindikiza nkhani kunja akusonyeza kuti mtsogoleri wa dziko la Uganda, Yoweri Museveni wasainila lamulo loletsa maukwati pakati pa amuna kapena akazi okha-okha; mchitidwe omwe umadziwika bwino kuti mathanyula.

Ofesi ya mtsogoleriyu komanso nyumba ya malamulo m’dzikolo akuti atsimikiza za nkhaniyi. Mwezi wathawu, aphungu a nyumba ya malamulo kumeneko adachita chimvano cha mavu pokanitsitsa kwamtu wa galu kuti mchitidwe wa mathanyula uyale mphasa mdzikolo.

Mwa zina, malamulo atsopanowa akuti munthu akangodziwika kuti akuchita mathanyula adzilandira chilango chokakhala ku ndende moyo wake onse.

Koma izitu zakwiyitsa maiko monga America komanso mabungwe ena omenyera ufulu wa anthu omwe akuti uku ndikuphwanya ufulu wa anthuwa Ngakhale zili chomwechi, mzika za ku Uganda zaikira kumbuyo President Museveni poima njii ndi ganizo lake losalola mchitidwe wa mathanyula. Iwo akuti izi zithandizira kuteteza chikhalidwe chawo.

Aliyense wopezeka akupititsa patsogolo mathanyula modziwa komanso mwadala adzimutumiza ku ndende kwa zaka 20. Ndipo mabungwe olimbikitsa m’chitidwewu adziwaletsa kugwira ntchito mdzikolo kwa zaka khumi.

Iyitu ndi nkhani yomwe atsogoleri ambiri muno mu Africa amachita nayo mantha kupereka maganizo awo poyera ati powopa kuthawitsa thandizo la ndalama kuchokera ku maiko olemera omwe ambiri mwa iwo saona vuto ndi mchitidwe wa mathanyula.

Pakadalipano, dziko la Malawi lili ndi nkhani ku bwalo la milandu komwe anthu awiri kuphatikizapo mkulu wina wa dziko la Netherlands akufuna oweruza milandu agamule kuti kuletsa mchitidwe wa mathanyula nkuphwanya malamulo akulu a dziko lino.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *