News

MWANAMVEKA AFUNIRA MAFUNO ABWINO A MALAWI PA NYENGO YA PASAKA

By Judgement Katika

Phungu wa nyumba Malamulo yemwe amayimira kumwera kwa boma la Chiradzulu, yemwenso akuyembekezeka kudzapikisana nawo pa mpando wa pulezident wa chipani cha Democratic Progressive Party(DPP) a Joseph Mathyola Mwanamvekha apereka uthenga wa mafuno abwino kwa a Malawi pamene akuyembekezeka kusangalalira phwando la pasaka mawa la chisanu.

Mu mkalata yemwo Mwanamvekha atulutsa la chinayi yati iyi ndi nthawi ya mtengo wapatali kuti a Malawi ayang’ane chitsogolo m’mayembekezo awo ndi kukhala ndi chithuzithuzi chakuwala limodzi ndi Yesu khirisitu .

Mwanamvekha anati : ” iyi ndi nthawi yokumbukira nsembe omwe Yesu khirisitu adadziperka kwa ife komanso kuti tikathe kudziyeretsanso mu chikhulupiriro, mkudzipereka kuchokera m’maphunziro yomwe iye atiphunzitsa pochiza ululu umene anthu amakumana nawo ndi kukhululuka.

” Pa nthawi ino ya chikondwerero cha pasaka chitibweretse pafupi ndi Mulungu ndipo tikapeze ufulu ndi mpumulo mu uthenga wa chiyembekezo ndi chipulumutso mu nyengo yoyera imene yabweretsa. ndikuyembekeza kuti uthenga umenewu wakupezani muli ndi moyo wabwino ndi mizimu ya pamwamba.”

Mwanamvekha anawonjezera popempha a Malawi kuti pamene akukondwerera nyengo ya Chimwemwe iyi ayenera kuti asiyiwale anthu amene anakhudzika ndi namondwe wa sayikoloni fulede pokondwerera nawo limodzi kupyolera mmachitachita a chifundo, kuwathandiza ndi ndalama komanso kuchiza ululu umene ali nawo.

Akhirisitu padziko lonse la pansi amakondwerera nyengo ya pasaka chaka ndi chaka ngati njira imodzi yokumbukira imfa ndi kuuka kwa Yesu Khirisitu.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *