News

MWANAMVEKA WAPELEKA THANDIZO LA CHAKUDYA KU MACHINGA

Olemba : Mtolankhani wanthu

Mmodzi mwa anthu omwe akufuna kudzapikisana nawo pa udindo wa mtsogoleri ku chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) Joseph Mwanamvekha, dzulo anayendera anthu okhudzidwawa m’boma la Machinga komwe anapereka thandizo la katundu osiyanasiyana.

Mwa zina, a Mwanamvekha anapereka zinthu monga, Nkhuku, ufa, nyemba, mazira, zakumwa, mkaka ma bisiketi ndi zakudya zosiyanasiyana kuphatikizapo ziwiya zotungira madzi.

Poyankhulapo, mfumu yaikuli Saidi Mataka yayamikira chifukwa cha thandizo lomwe a Mwanamvekha apereka pozindikira kuti ndi ochepa omwe angachite zimenezi, ndipo mfumuyi yapempha boma kuti lithandizeponso ndi chakudya pozindikira kuti zokolola zosiyanasiyana kuphatikizapo mpunga, zinaonongeka ndi namondweyo komanso pakuyenera kuwathandizanso ndi zipangizo zomangira pozindikira kuti alibe pokhala.

Kumbali yake phungu wadera la pakati pa boma la Machinga, Daudi Chikwanje wati zomwe achita a Joseph Mwanamvekha ndi zinthu zokondweretsa poti ili ndi thandizo loyamba kubwera ku derali ndipo walonjeza anthu kuti agwira ntchito ndi a Mwanamvekha.

Mmawu ake, Joseph Mwanamvekha walonjeza anthu omwe anasonkhana pamalowa kuti apitiriza kuthandizana ndi phungu wa derali.
Mwanamvekha anatinso sasiira pomwepa kugwira ntchito yothandiza anthu omwe anakhuzidwa ndi namondwe wa Freddy.

A Mwanamvekha akhalanso akuyendera ena mwa madera omwe anakhudzidwa ndi namondwe wa Freddy yemwe wapha anthu opitirira 500 komanso kuononga mbewu, ziweti, katundu wa anthu osiyanasiyana, misewu m’maboma amchigawo cha ku mmwera kwa dziko lino.

Mwa ena omwe anabwela ndi Mafumu monga awa Agrupu Amalaka ,Amosha, Amuhaniwa,Khuzumba ndi Chilala ndi ena

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *