News

MWIKHO! BAMBO AGONANA NDI MAI WAMISALA

Olemba: Mtolankhani wanthu

Apolisi ku Lilongwe akusunga mchitokosi bambo wa zaka 39, Dackson Gabriel ati kaamba kochita zachiwerewere ndi m’mai wina yemwe akuti mutu wake sugwira bwino-bwino.

Mneneri wa polisi ya Kanengo, Gresham Ngwira wati m’maiyu adakumana ndi Gabriel ku Nsungwi usiku wina koma adamuuza kuti akusowa malo ogona.

Apa, akuti Gabriel adamuuza m’maiyu kuti asadandaule amutengera ku nyumba kwake komwe akagone chipinda chimodzi ndi mkazi wake.

Malingana ndi Ngwira, oganizilidwayu ankanama kuti ali mkazi ndipo mu usikuwu adachita za dama ndi m’maiyu kawiri konse.

“Kutacha, m’maiyu adasakasaka mkulu wa derali komwe adakatula nkhani yonse ndipo achitetezo akudera adagwira Gabriel ndikukamutula ku Nsungwi Police Unit,” watero Ngwira.

Gabriel amachokera m’boma la Mchinji ndipo akuyembekezeka kuyankha mulandu ochita za dama ndi munthu yemwe mutu wake sugwira bwino zomwe nzosemphana ndi gawo 139 la malamulo.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *