NationalNews

MZIKA ZAKU ZAMBIA AZIGAMULA ZAKA 6 KUKASWEZA NDENDE

Mtolankhani wanthu

Bwalo la milandu la First Grade Magistrate ku Kasungu lagamula nzika ziwili za dziko la Zambia kuti zikaseweze jele kwa zaka zisanu mchimodzi zitapezeka ndi mnyanga wa njovu zomwe mzosemphana ndi gawo 86 (1) la nyama zotetezeka.

Yemwe anaimira nthambi ya nyama za kutchile pa mlanduwu a Mtheto Ndhlamini aku Kasungu National Park ati awiliwa ndi bambo wa ulumali osaona a Cosmas Phiri a zaka 68 ndi Malani Phiri wa zaka 30.

A Ndhlamini ati awiriwa adawamanga pa 27 November chaka chatha ku Nkhamenya atapezeka ndi mnyanga wa njovu wolemera ma kilogilamu 20.1 womwe amafuna kukagulitsa ku Lilongwe kapena ku Mangochi.

“Awiliwa atawonekera ku bwalo la milandu koyamba adauvomera mlanduwu ndipo adapempha bwalo kuti liwamvere chisoni poti nkoyamba kupalamula mlanduwu komanso poti wopalamula woyamba (Cosmas) ali ndi ulumali,” atero a Ndhlamini.

Komatu woimira boma pa mlanduyu anapempha bwalo kuti liwapatse chilango chokhwima awiliwa poti mchitidwe wopha nyama mu nkhalango yotetezeka ya Kasungu wakula kwambili.

Apa, oweluza mlanduwu, Damiano Banda adagwilizana ndi pempholi ponena kuti ulumali sikulephera kotero wagamula awiliwa kukaseweza jele kwa zaka zisanu mchimodzi.

Awiliwa amachokera m’mudzi wa Chimwazimwazi mfumu yaikulu Mwasenthembwe m’boma la Lundazi ku Zambia.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *