News

NZIKA YAKU INDIA YAGWILILA MWANA WA ZAKA 5

Mtolankhani Wanthu

Bambo wa zaka 57 zakubadwa, Ramsigng Narissing Shinde yemwe ndi mzika ya ku India, ili mchitokosi cha apolisi ku Limbe mu mzinda wa Blantyre pomuganizira kuti wagwilira mwana wa zaka 5.

Wofalitsa nkhani pa polisi ya Limbe, Aubrey Singanyama watiwuza kuti mkuluyu akuganizilidwa kuti anapalamula mlanduwu Lamulungu lapitali ku nyumba kwake ku Maone.

Ad: Studio Combo

“Mkuluyu anayitanira ku chipinda mwanayu pamodzi ndi mchemwali wake wa zaka 6 powanyengelera ndi chapati. Apa anawavula zovala zonse ndipo pambuyo pake anapalamula mlanduwu,” atero a Singanyama.

Apa, malingana ndi ofalitsa nkhani za polisi ya Limbe-yu, ndi pomwe mchimwene wawo wa anawa analowa mchipinda momwe amachitira izi ndipo anamupezelera Shinde akuchita kusaweruzikaku.

Kenaka, nkhaniyi anaitengera kwa makolo a anawa za nkhaniyi omwe sanachedwe koma kukamuneneza ku polisi.

Shinde aonekera m’bwalo la milandu mawa, Lachisanu komwe akayankhe mlandu ogwililira.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *