NationalNews

OLEMEKEZEKA A NAVICHA ALIPILILA OPHUNZIRA ONSE MDERA LAWO NDALAMA YA MAYESO

By Judgement Katika

Phungu wa ku Nyumba ya Malamulo KU dera la Thyolo Thava, Wolemekezeka Mai Mary Thom Navicha, walipira ndalama za mayeso za ophunzira wonse KU dera lawo la Thyolo Thava omwe akuyembekezera kulemba mayeso a STD 8, JCE komanso MSCE amene sanakwanitse kulipira ndalama ya mayeso ku MANEB kamba Ka umphawi.

Phunguyu wati wachita izi poganizira nyengo zovuta zimene makolo a ophunzirawa akudutsamo.

” Monga mukudziwa kuti nthawi yatsala pang’ono kuti a MANEB atseke kulandira ndalamazi, ndawona kuti ndiwathangate makolo omwe pakadali pano akuvutika mwadzaoneni kuti apeze ndalama! Pakadali pano, Kuli njala yowopsa ndipo izi zapangitsa makolo ambiri kulephera kupeza ndalama yolipirira mayesowa! Ndikupemphanso ena akufuna kwambwino kuti tithandizane kulipilira ana ena omwe sanakwanitsebe kulipira ndalamayi” Atero Mai Navicha.

Pakadali pano Iwo afotokoza kuti apitiliza kupempha Boma kuti iganizire a Malawi wosowa ochuluka powapeputsa maka nthawi ino pamene kugwa kwa ndalama ya kwacha komanso njala zakhudza kwambiri mawanja awo.

” Nkhani ina yomvetsa chisoni ndiyakuti ngakhale sukulu yatsegulira, makolo ambiri wovutika sakudziwa kuti fizi akayitenga kuti. Ngakhale Kuli ndondimeko zina zofikira ana amene ali wovutika, ndondomekozi sizikukwanitsa kufikira ana wonse.” Anadandaula motero Mai FC Navicha omwe ndi Wamkulunso Wotsogolera Amai mu chipani cha DPP.

Kuyambira kalekale, phunguyu wakhala akuthandiza Wophunzira amene amamufikira ndi mavuto osiyanasiyana koma Lero potengera kuchiluka kwa ophunzira wofunika kuthandizidwa, anaganiza zongofikira wonse.

Bungwe la MANEB linawonjezera masiku anayi kuti ophunzira woposa 29,000 omwe anali asanalipirebe ndalama ya mayeso alipire.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *