News

OPHUNZIRA STD7 WAPHA MZAKE PANDEWU YOLIMBILANA CHIBWEDZI

Mtolankhani wanthu

Apolisi ku Machinga ati akusakasaka ophunzira wa Standard 7, Chikondi Dailesi, 14, wa pa sukulu ya pulaimale ya Chikweo m’boma la Machinga pomuganizira kuti wapha mzake, Victor Biziweck, 12 wa Standard 4.

Mneneri wa polisi ku Machinga Western Kansire watsimikiza za nkhaniyi.

Iwo ati anyamata awiriwa adali pa ubwenzi ndi mtsikana m’modzi koma samadziwana kufikila Lachisanu lapitali.

“Izi zidapangitsa kuti anawa ayambe kumenyana ndipo Victor adagwa pansi nkukomoka. Victor adamwalira atafika kuchipatala cha Chikweo ndipo azaumoyo atamuyeza adampeza ndi nthenda ya malungo komanso kuchepa kwa magazi mthupi mwake,” watero Kansire.

Pakadali pano, Kansire wati apolisi sakudziwa komwe kunathawira Chikondi Dailesi ndipo monga mwa ntchito yawo ali mkati momusakasaka.

Chikondi amachokera m’mudzi mwa Mkolimbo mdera la mfumu yaikulu Chikweo ndipo Victor ankachokera m’mudzi mwa mfumu Manja mdera la mfumu yaikulu Chikweo m’boma lomweli la Machinga.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

One thought on “OPHUNZIRA STD7 WAPHA MZAKE PANDEWU YOLIMBILANA CHIBWEDZI

  • Your articles are extremely helpful to me. Please provide more information!

    Reply

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *