News

PALIBENSO KUONETSA CHIPHASO CHA KATEMERA WA COVID

Mtolankhani Wanthu

Komiti yoona za matenda a Covid-19 m’dziko muno yati kuonetsa chiphaso choti munthu analandira katemera wa nthendayi polowa kapena kutuluka m’dziko muno sikukhalanso kokakamiza tsopano.

Wapampando wa komitiyi yemwenso ndi nduna ya za umoyo, Khumbize Kandodo Chiponda watsimikiza izi.

Koma iye wapempha aMalawi kuti apitilizebe kutsatira njira zodzitetezera ku matendawa kaamba koti matendawa adakalipo m’dziko muno.

Izi zikutsatira kulengeza kwa bungwe loona za umoyo pa dziko lonse la WHO miyezi yapitayo kuti nthendayi siodetsanso nkhawa pakadalipano.

“Ngakhale zili chomwechi, katemera wa Covid-19 adziperekedwabe m’zipatala za m’dziko muno,” watero Chiponda.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *