News

SITIKULANDILA MALIPIRO ANTHU , ANDAWULA OGWIRA NTCHITO KU MCHINJI

By The Radar, online publicationKulephera kwa udindo wake opeleka ukhondo mmisika ina ya boma la Mchinji kwakhudza nkhani zachuma pa khosolo la bomali; pomwe ogwila ntchito ena akuti kufikira lero sanalandile malipiro awo a miyezi isanu kuchokera mu November chaka chatha.

Anthu-wa, omwe sanafune kuti tiwatchule maina atiuza kuti nthawi zambiri vutoli likagwa amadulidwa malipiro awo.

“Tikulephera kulipila nyumba zomwe tikukhala, moti tikugwa mu ngongole zomwe mapeto ake tikulandidwa katundu ndi a ngongole ngakhaleso eni nyumba-zo,” atero ena mwa ogwira ntchito-wo.

Wapampando wa makhasala ku Mchinji, Dennis Lazaro, watsutsa kuti anthuwa atha miyezi isanu asakulandila malipiro awo, ponena kuti ofesi yake ikudziwa za miyezi itatu yomwe anthuwa akhala akulandira theka la malipiro awo.

Mkulu wa komiti ya zachuma ku khonsolo ya bomali, Kennedy Chipanga, watsimikiza kuti chuma cha khosoloyi chasokonekela kutsatira kunyanyala kwa umodzi wa misika ikuluikulu wa Kamwendo komwe ochita malonda akhala akunyanyala kupereka msonkho wa tsiku ndi tsiku.

Ndipo wachiwiri kwa wapampando wa msika wa Kamwendo, Abdul Maliko, wati ochita malonda akunyanyala kupereka msonkho-wo kaamba koti chimbudzi cha msika-wo chinagwa mu September, 2021.

Pano, ntchito yomanga-nso chimbudzi-cho ili mkati koma ochita malonda pa msika-wo, akuti akufuna zokambirana zawo zina ndi akuluakulu a khonsolo ya Mchinji zifike kumapeto, asanayambire-nso kupereka msonkho-wo.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *