News

TIYENI TILILE AZANTHU OMWE AMWALILA KAMBA KA NAMONDWE, APEMPHA APULEZIDENTI

By Cy’rus Bengo

Mtsogoleli wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wapempha a Malawi kuti akhale masiku khumi ndi anayi, 14 olira anzathu omwe amwalira kaamba ka namondwe wotchedwa Freddy.

A Chakwera kukhuza maliro ku BT

Dr. Chakwera anayankhula izi mu uthenga wake wapadera ku mtundu wa a Malawi.

Mwazina iwo ati mbendera za dziko lino zikhale zotsika kwa masiku 7 akudzawa.

Iwo anapitiliza kupempha a Malawi onse kuti amange umodzi ndi kuthandizana mu nthawi ya zovutayi.

A Chakwera atinso akhalabe mu m’zinda wa Blantyre pofuna kuyendetsa ntchito yothandiza anthu omwe akhudzidwa.

“Nditayendera madera ochuluka omwe kukukhala anthu asungidww mongoyembekedzera ndamva chisoni kwambiri choncho nkofunika thandizo la nsanga” Iwo anatero.

Potsilizira Dr Chakwera apempha akufuna kwabwino kuti asaleme pa ntchito yabwino yomwe ayamba kale pothandiza abale omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.

Naye mtsogoleri wakale wadziko lino Peter Mutharika wapempha umodzi pakati pa a Malawi kuti ntchito yothandiza anthu omwe akhudzidwa ndi namondweyu iyende bwino.

A Mutharika anayankhula izi pomwe amayendera ena ma madera omwe anthu omwe akusowa kokhalawa akusungidwa.

Wachitatu kumadzere ndi mtsogoleri wakale Mutharika

Malingana ndi a Mutharika anthu asalowetse ndale pa ngoziyi koma akhale ndi mtima ongothandiza.

Pa ulendowu mtsogoleri wakeleyu anapereka ma bulangete, ufa, nyemba komanso katundu wina.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *