News

WAMWALIRA MKATI MOSANGALALA NDI WACHIKONDI WAKE KUMALO OGONA ALENDO

Mtolankhani wanthu

Mwamuna wazaka za mma 70 wapezeka atafa kumalo ogona alendo ku Chitakale m’boma la Mulanje, pomwe zadziwikanso kuti anali ndi mkazi wachibwenzi.

Mneneri wapolisi ku Mulanje, Innocent Moses, wati bamboyo, yemwe dzina lake ndi Lemon Walama, amagwira ntchito ngati wachitetezo pamalopo. Malinga ndi a Moses, malemuwo anapeza mkazi wachibwenzi ndipo analowa naye mchipinda cha pamalopo kuti akasangalale ndipo anamwa mankhwala owonjezera chisangalalo.

Mmawa watsiku lotsatira, bamboyo anapezeka atafa ndipo zotsatira zachipatala zasonyeza kuti bamboyo wamwalira chifukwa cha matenda a mtima omwe anayamba chifukwa cha kuthamanga kwa magazi kaamba ka mankhwala owonjezera chisangalalo anamwawo. Pakadali pano, mkaziyo ali mmanja mwa apolisi kuti afotokoze zambiri zankhaniyi.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *