News

WAPOLISI WAMWA MAGALASI KU THYOLO POFUNA KUNZIPHA

Mtolankhani wanthu

Wapolisi wina ku Thyolo, Constable Elson Mnyalira akubuwula ndi ululu wadzaoneni mchipatala chachikulu cha m’bomali atabwira magalasi pothawa unyolo atatentha mkazi wake ndi madzi owotcha.

Mneneri wa polisi mchigawo cha kummwera chakumvuma, Edward Kabango wati Mnyalira anakangana ndi bwenzi lake, Tumelo Banda.

Malipoti akuti panthawiyo mkuti mkuluyu akuchokera kopsontha bibida dzulo pa 25 August.

“Kutsatira mkanganowu, a Mnyalira anathira madzi otentha mkhosi mwa nthiti yawoyi. Apatu, uthenga unapita ku polisi ya Luchenza ndipo apolisi anayamba dongosolo lofuna kunjata a Mnyalira,” watero Kabango.

Atamva izi, mkulu wa chipewa cha phalayu akuti anaganiza zokumwa magalasi ati pofuna kudzipha.

Komatu izi sizingatheke popeza anthu anamupulumutsa mkuluyu mkumutengera ku chipatala cha Thyolo komwe anamugoneka.

A Mnyalira amagwira ntchito ngati wapolisi ku Police Mobile Service ku G Division.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *