News

WAZIPHA ATASEMPHANITSA ZIZIMBA

Mtolankhani wanthu

Mnyamata wa zaka 21 Felix Chikhasu wadzipha podziponya ku galimoto yomwe idali pa liwiro Loweluka pa malo otchedwa Ndagoma m’mbali mwa msewu wa M1 ku Ntcheu.

Mneneri wa a polisi ku m’bomali, Rabecca Ndiwate wati Chikhasu adauza anzake kuti adapita kwa sing’anga kukatenga zitsamba kuti alemele koma wasemphanitsa zizimba.

Atazindikira kuti wasemphanitsa zizimbazi, m’nyamatayu akuti adaganiza zodzipha kusiyana mkuti achite misala monga momwe ng’angayi idamuchenjezera.

“Lachisanu, Chikhasu adamwa mankhwala kuti adziphe ma anthu adamutengera kuchipatala komwe adamugoneka.

“Loweluka, anathawa mchipatalamu mkukadziponya ku galimoto ndipo anthu anamutengeraso ku chipatala komweko komwe wamwalira kamba kovulala kwambili m’mutu,” watero Ndiwate.

Chikhasu ankachokera m’mudzi wa Gwaza mfumu yaikulu Ganya m’boma la Ntcheu.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *