NationalNews

ZAKA 10 KU NDENDE KWA MSILIKALI OPUMA , KAMBA KAKUBA

Mtolankhani wanthu

Bwalo la mlandu la Senior Resident ku Lilongwe lagamula msilikali wakale wa Malawi Defense Force Precious Khonje kukaseweza zaka 10 ku ndende kamba koba moophyeza.

Mneneri wa polisi ya Lilongwe Hastings Chigalu wati Khonje anamangidwa mwezi wa June chaka chatha kutsatira kuba moophyeza komwe anachita ku Airwing, Njewa mumzinda wa Lilongwe.

Oyimira boma pa mulanduwu, Vincent Ntalawe akuti Khonje anali ndi anzake asanu ndi anayi ndipo anamanga mlonda ndi kuthyola nyumba pomwe anaba wailesi za kanema ziwiri, lamya, ndalama ndi zinthu zina zomwe zimakwana K1.6 million.

Khonje anauza anzake kuti amenye maliseche a mlondayo yemwenso amaphuphaphupha pa nthawiyo.

“Koma Khonje anamangidwa ndi a chitetezo adera usiku womwewo pomwe anzake anathawa. Ndipo munthuyi anakana mlanduwu, koma boma linabweretsa mboni zisanu ndi ziwiri zomwe zinatsimikiza kuti Khonje ndi wakuba,” watero Chigalu.

Ndipo ogamula mlanduwu Shukran Kumbani anagamula kuti a Khonje akakhale ku ndende kwa zaka 10.

Precious Khonje amachokera mmudzi mwa Namalita, TA Mwambo ku Zomba.

Team Plus TV

We are a digital TV station that videocast live events and news as it come into being which we publish across all formats biginning with this platform, we hope to appeal to the bulk of young and middle class elites with a vision of the future and belief in a social change. Pin on delivering fresh , factual and reliable news . We offer the fastest and deepest journalism, it is one stop media portal with high standards in content creation. Our primary value is our audience thus creating relevant content that matters.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *